3 Pamenepo Yudase yemwe anampereka Iye, poona kuti Iye anatsutsidwa kuti afe, analapa, nabweza ndalama zija zasiliva makumi atatu kwa ansembe akuru ndi akuru,
4 nanena, Ndinacita koipa ine, pakupereka mwazi wosalakwa. Koma iwo anati, Tiri naco ciani ife? udzionere wekha.
5 Ndipo iye anataya pansi ndalamazo paKacisi, nacokapo, nadzipacika yekha pakhosi.
6 Ndipo ansembe akuru anatenga ndalamazo, nati, Sikuloledwa kuziika m'cosonkhera ndalama za Mulungu, cifukwa ndizo mtengo wa mwazi.
7 Koma anapangana, nazigula munda wa woumba mbiya, ukhale manda a alendo.
8 Cifukwa cace munda umenewu anaucha, Munda-wa-mwazi, kufikira lero lino.
9 Pamenepo cinakwaniridwa conenedwa ndi Yeremiya mneneri, ndi kuti,Ndipo iwo anatenga ndalamazo zasiliva makumi atatu,Mtengo wa uja wowerengedwa mtengo wace,Amene iwo a ana a Israyeli anawerenga mtengo wace;