5 Pamenepo panamturukira iye ku Yerusalemu, ndi Yudeya lonse, ndi dziko lonse loyandikana ndi Yordano;
6 nabatizidwa ndi iye mu mtsinjewo wa Yordano, alikuulula macimo ao.
7 Ndipo iye pakuona ambiri a Afarisi ndi a Asaduki akudza ku ubatizo wace, anati kwa iwo, Obadwa a njoka inu, ndani anakulangizani kuthawa mkwiyo ulinkudza?
8 Onetsani inu zipatso zakuyenera kutembenuka mtima:
9 ndipo musamayesa kunena mwa inu nokha, Atate wathu tiri naye Abrahamu; pakuti ndinena kwa inu kuti mwa miyala iyi Mulungu akhoza kuukitsira Abrahamu ana.
10 Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo; cifukwa cace mtengo uli wonse wosabala zipatso zabwino udulidwa nuponyedwa pamoto,
11 Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zace: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto: