11 Comweco, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye?
12 Cifukwa cace zinthu ziri zonse mukafuna kuti anthu acitire inu, inunso muwacitire iwo zotero; pakuti ico ndico cilamulo ndi aneneri.
13 Lowani pa cipata copapatiza; cifukwa cipata ciri cacikuru, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka iri yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa ico.
14 Pakuti cipata ciri copapatiza, ndi icepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akucipeza cimeneco ali owerengeka.
15 Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zobvala zankhosa, koma m'kati mwao ali afisi alusa.
16 Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi achera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula?
17 Comweco mtengo wabwino uli wonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuci upatsa zipatso zoipa,