14 Pomwepo anadza kwa Iye ophunzira ace a Yohane, nati, Cifukwa ninji ife ndi Afarisi tisala kudya kawiri kawiri, koma ophunzira anu sasala?
15 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? koma adzafika masiku, pamene mkwati adzacotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.
16 Ndipo kulibe munthu aphathika cigamba ca nsaru yaiwisi pa copfunda cakale; pakuti cigamba cace cizomoka ku copfundaco, ndipo cicita ciboo cacikuru.
17 Kapena samathira vinyo watsopano m'matumba akale; akatero, matumba aphulika, ndi vinyo atayika, ndi matumba aonongeka: koma athira vinyo watsopano m'matumba atsopano, ndi zonse ziwiri zisungika.
18 M'mene Iye analikulankhula nao zinthu zimenezo, onani, anadza munthu mkuru, namgwadira Iye, nanena, Wamwalira tsopanolimwana wanga wamkazi, komatu mudze muike dzanja lanu pa iye, ndipo adzakhala ndi moyo.
19 Ndipo Yesu ananyamuka namtsata iye, ndi ophunzira ace omwe.
20 Ndipo onani, mkazi, anali ndi nthenda yacidwalire zaka khumi ndi ziwiri, anadza pambuyo pace, nakhudza mphonje ya copfundacace;