9 Ndi ana a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Rama, ndi Sabteka. Ndi ana a Rama: Seba, ndi Dedani.
10 Ndi Kusi anabala Nimmdi; iye anayamba kukhala wamphamvu pa dziko.
11 Ndi Mizraimu anabala Aludi, ndi Aanami, ndi Alehabi, ndi Anaftuki,
12 ndi Apatrusi, ndi Akasluki, (kumene anafuma Afilisti), ndi Akafitori.
13 Ndi Kanani anabala Zidoni mwana wace woyamba, ndi Heti,
14 ndi Ayebusi, ndi Aamori, ndi Agirigasi,
15 ndi Ahivi, ndi Aariki, ndi Asini,