28 Ndi ana a Onamu ndiwo Samai, ndi Yada; ndi ana a Samai: Nadabu, ndi Abisuri.
29 Ndipo dzina la mkazi wa Abisuri ndiye Abihaili; ndipo anambalira Abani, ndi Molidi.
30 Ndi ana a Nadabu: Seledi ndi Apaimu; koma Seledi anamwalira wopanda ana.
31 Ndi mwana wa Apaimu: lsi. Ndi mwana wa lsi: Sesani. Ndi mwana wa Sesani: Alai.
32 Ndi ana a Yada mbale wa Samai: Yeteri, ndi Yonatani; namwalira: Yeteri wopanda ana.
33 Ndi ana a, Yonatani: Peleti, ndi Zaza. Ndiwo ana a Yerameli.
34 Ndipo Sesani analibe ana amuna, koma ana akazi. Ndi Sesani anali naye mnyamata M-aigupto dzina lace ndiye Yara.