31 Ndi mwana wa Apaimu: lsi. Ndi mwana wa lsi: Sesani. Ndi mwana wa Sesani: Alai.
32 Ndi ana a Yada mbale wa Samai: Yeteri, ndi Yonatani; namwalira: Yeteri wopanda ana.
33 Ndi ana a, Yonatani: Peleti, ndi Zaza. Ndiwo ana a Yerameli.
34 Ndipo Sesani analibe ana amuna, koma ana akazi. Ndi Sesani anali naye mnyamata M-aigupto dzina lace ndiye Yara.
35 Ndipo Sesani anampatsa Yara mnyamata wace mwana wace wamkazi akhale mkazi wace, ndipo anambalira Atai.
36 Ndipo Atai anabala Natani, ndi Natani anabala Zabadi,
37 ndi Zabadi anabala Efilali, ndi Efilali anabala Obedi,