6 Ndi ana a Zera: Zimri, ndi Etani, ndi Hemani, ndi Kalikoli, ndi Dara; onse pamodzi ndi asanu.
7 Ndi ana a Karmi: Akari wobvuta Israyeliyo, amene analakwira coperekedwa ciperekereco.
8 Ndi mwana wa Etani: Azariya.
9 Ndi ana a Hezironi anambadwirawo: Yerameli, ndi Ramu, ndi Kelubai.
10 Ndi Ramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Nasoni kalonga wa ana a Yuda;
11 ndi Nasoni anabala Salima, ndi Salima anabala Boazi,
12 ndi Boazi anabala Obedi, ndi Obedi anabala Jese,