8 Ndi mwana wa Etani: Azariya.
9 Ndi ana a Hezironi anambadwirawo: Yerameli, ndi Ramu, ndi Kelubai.
10 Ndi Ramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Nasoni kalonga wa ana a Yuda;
11 ndi Nasoni anabala Salima, ndi Salima anabala Boazi,
12 ndi Boazi anabala Obedi, ndi Obedi anabala Jese,
13 ndi Jese anabala mwana wace wamwamuna woyamba Eliabu, ndi Abinadabu waciwiri, ndi Simeya wacitatu,
14 Netaneli wacinai, Radai wacisanu,