1 Pamenepo Davide anasonkhanitsa ku Yerusalemu akalonga Israyeli, a akalonga a mapfuko, ndi akuru a zigawo zakutumikira mfumu, ndi akulu a zikwi, ndi akuru a mazana, ndi akuru a zolemera zonse, ndi zoweta zonse za mfumu, ndi ana ace; pamodzi ndi akapitao ndi anthu amphamvu, ndiwo ngwazi zamphamvu onsewo.
2 Ndipo mfumu Davide anaima ciriri, nati, Mundimvere ine, abale anga ndi anthu anga, ine kumtima kwanga ndinafuna kulimangira likasa la cipangano la Yehova, ndi popondapo mapazi a Mulungu wathu nyumba yopumulira, ndipo ndidakonzeratu za nyumbayi.
3 Koma Mulungu anati kwa ine, Sudzamangira dzina langa nyumba, popeza ndiwe munthu wa nkhondo wokhetsa mwazi.
4 Komatu Yehova Mulungu wa Israyeli anasankha ine m'nyumba yonse ya atate wanga, ndikhale mfumu ya Israyeli kosatha; pakuti anasankhiratu Yuda akhale mtsogoleri, ndi m'nyumba ya Yuda nyumba ya atate wanga, ndi mwa ana a atate wanga ndinamkomera ndine, andilonge ufumu wa Israyeli yense;
5 ndi mwa ana anga onse (pakuti Yehova wandipatsa ana amuna ambiri), anasankha Solomo mwana wanga akhale pa mpando wacifumu wa ufumu wa Yehova kuweruza Israyeli.
6 Ndipo anati kwa ine, Solomo mwana wako ndiye adzandimangira nyumba yanga ndi mabwalo anga; pakuti ndamsankha akhale mwana wanga, ndipo Ine ndidzakhala atate wace.
7 Ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wace kosatha, akalimbika kucita malamulo anga ndi maweruzo anga monga lero lino.