3 wacisanu Sefatiya wa Abitali, wacisanu ndi cimodzi Itreamu wa mkazi wace Egila,
4 Anambadwira asanu ndi mmodzi m'Hebroni; ndi pomwepo anakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri, ndi miyezi isanu ndi iwiri; ndi m'Yerusalemu anakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu zitatu.
5 Ndipo ombadwira m'Yerusalemu ndi awa: Simeya, ndi Sobabu, ndi Natani, ndi Solomo, anai a Batisuwa mwana wamkazi wa Amieli;
6 ndi Ibara, ndi Elisama, ndi Elifeleti,
7 ndi Noga, ndi Nefegi, ndi Yafiya,
8 ndi Elisama, ndi Eliada, ndi Elifeleti, asanu ndi anai.
9 Onsewa ndiwo ana a Davide, pamodzi ndi ana a akazi ang'ono; ndipo Tamara ndiye mlongo wao.