14 ndi Azariya anabala Seraya, ndi Seraya anabala Yehozadaki,
15 ndi Yehozadaki analowa undende muja Yehova anatenga ndende Yuda ndi Yerusalemu ndi dzanja la Nebukadinezara.
16 Ana a Levi: Gerisomu, Kohati ndi Merari.
17 Ndipo maina a ana a Gerisomu ndi awa: Libni, ndi Simei.
18 Ndipo ana a Kohati ndiwo Amramu, ndi lzara, ndi Hebroni, ndi Uzieli.
19 Ana a Merari: Mali ndi Musi. Ndi mabanja a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao ndi awa.
20 Wa Gerisomu: Libni mwana wace, Yahati mwana wace, Zina mwana wace,