42 mwana wal Edani, mwana wa Zima, mwana wa Simeyi,
43 mwana wa Yabati, mwana wa Gerisomu, mwana wa Levi.
44 Ndi ku dzanja lamanzere abale ao ana a Merari: Etani mwana wa Kisi, mwana wa Abidi, mwana wa Maluki,
45 mwana wa Hasabiya, mwana wa Amaziya, mwana wa Hilikiya,
46 mwana wa Amzi, mwana wa Bani, mwana wa Semeri,
47 mwana wa Mali, mwana wa Musi, mwana wa Merari, mwana wa Levi.
48 Ndi abale ao Alevi anaikidwa acite za utumiki ziti zonse za kacisi wa nyumba ya Mulungu.