53 Zadoki mwana wace, Ahimaazi mwana wace.
54 Pokhala pao tsono monga mwa madera ao m'malire mwao ndi awa: kwa ana a Aroni a mabanja a Akobati, pakuti maere oyamba adagwera iwowa,
55 kwa iwo anapereka Hebroni m'dziko la Yuda, ndi podyetsa pace pozungulira pace;
56 koma minda ya mudzi ndi miraga yace anapatsa Kalebi mwana wa Yefune.
57 Ndi kwa ana a Aroni anapereka midzi yopulumukirako: Hebroni, ndi Libina ndi mabusa ace, ndi Yatiri, ndi Esitemowa ndi mabusa ace,
58 ndi Hileni ndi mabusa ace, ndi Debiri ndi mabusa ace,
59 ndi Asani ndi mabusa ace, ndi Betesemesi ndi mabusa ace;