77 Otsala a Alevi analandira, motapa pa pfuko la Zebuluni, Rimono ndi mabusa ace, Tabora ndi mabusa ace;
78 ndi tsidya lija la Yordano kum'mawa kwa Yordano analandira, motapa pa pfuko la Rubeni, Bezeri m'cipululu ndi mabusa ace, ndi Yaza ndi mabusa ace,
79 ndi Kedemoti ndi mabusa ace, ndi Mefati ndi mabusa ace;
80 ndi motapa m'pfuko la Gadi, Ramoti m'Gileadi ndi mabusa ace, ndi Mahanaimu ndi mabusa ace,
81 ndi Hezboni ndi mabusa ace, ndi Yazeri ndi mabusa ace.