9 ndi Ahimaazi anabala Azariya, ndi Azariya anabala Yohanani,
10 ndi Yohanani anabala Azariya (ndiye amene anacita nchito ya nsembe m'nyumba anaimanga Solomo m'Yerusalemu),
11 ndi Azariya anabala Amariya, ndi Amariya anabala Ahitubu,
12 ndi Ahitubu anabala Zadoki, ndi Zadoki anabala Salumu,
13 ndi Salumu anabala Hilikiya, ndi Hilikiya anabala Azariya,
14 ndi Azariya anabala Seraya, ndi Seraya anabala Yehozadaki,
15 ndi Yehozadaki analowa undende muja Yehova anatenga ndende Yuda ndi Yerusalemu ndi dzanja la Nebukadinezara.