2 Noha wacinai, ndi Rafa wacisanu.
3 Ndi Bela anali ndi ana: Adara, ndi Gera, ndi Abihudi,
4 ndi Abisuwa, ndi Namani, ndi Ahowa,
5 ndi Gera, ndi Sefufani, ndi Huramu.
6 Ndi ana a Ehudi ndi awa: ndiwo akuru a nyumba za makolo ao a iwo okhala ku Geba, ndipo anawatenga ndende kumka ku Manahati,
7 natenga ndende Namani, ndi Ahiya, ndi Gera, ndipo, anabala Uza, ndi Ahihudi.
8 Ndipo Saharaimu anabala ana ku dziko la Moabu, atacotsa akazi ace Husimu ndi Baara.