26 ndi Samserai, ndi Sehariya, ndi Ataliya,
27 ndi Yaaresiya ndi Eliya, ndi Zikiri, ana a Yerohamu.
28 Awa ndi akuru a nyumba za makolo mwa mibadwo yao, ndiwo akuru anakhala m'Yerusalemu awa.
29 Ndipo m'Gibeoni anakhala atate a Gibeoni, dzina la mkazi wace ndiye Maaka;
30 ndi mwana wace woyamba ndiye Abidoni, opondana naye ndi Zuri, ndi Kisi, ndi Baala, ndi Nadabu,
31 ndi Gedoro, ndi Ahiyo, ndi Zekeri.
32 Ndipo Mikiloti anabala Simeya. Ndi iwonso anakhala pamodzi ndi abale ao m'Yerusalemu, popenyana ndi abale ao.