28 Awa ndi akuru a nyumba za makolo mwa mibadwo yao, ndiwo akuru anakhala m'Yerusalemu awa.
29 Ndipo m'Gibeoni anakhala atate a Gibeoni, dzina la mkazi wace ndiye Maaka;
30 ndi mwana wace woyamba ndiye Abidoni, opondana naye ndi Zuri, ndi Kisi, ndi Baala, ndi Nadabu,
31 ndi Gedoro, ndi Ahiyo, ndi Zekeri.
32 Ndipo Mikiloti anabala Simeya. Ndi iwonso anakhala pamodzi ndi abale ao m'Yerusalemu, popenyana ndi abale ao.
33 Ndipo Neri anabala Kisi, ndi Kisi anabala Sauli, ndi Sauli anabala Yonatani, ndi Malikisuwa, ndi Abinadabu, ndi Esibaala.
34 Ndi mwana wa Yonatani ndiye Meri-baala; ndi Meri-baala anabala Mika.