6 Ndi ana a Ehudi ndi awa: ndiwo akuru a nyumba za makolo ao a iwo okhala ku Geba, ndipo anawatenga ndende kumka ku Manahati,
7 natenga ndende Namani, ndi Ahiya, ndi Gera, ndipo, anabala Uza, ndi Ahihudi.
8 Ndipo Saharaimu anabala ana ku dziko la Moabu, atacotsa akazi ace Husimu ndi Baara.
9 Ndipo Hodesi mkazi wace anambalira Yohabu, ndi Zibiya, ndi Mesa, ndi Malikamu,
10 ndi Yeuzi, ndi Sakiya, ndi Mirima. Awa ndi ana ace akurua nyumbazamakolo ao.
11 Ndi Husimu anambalira Abitubu, ndi Elipaala.
12 Ndi ana a Elipaala: Eberi, ndi Misamu, ndi Semedi, amene anamanga Ono, ndi Ludi ndi miraga yace,