38 Ndi Mikiloti anabala Simeamu. Ndipo iwonso anakhala pamodzi ndi abale ao m'Yerusalemu, pandunji pa abale ao.
39 Ndipo Neri anabala Kisi, ndi Kisi anabala Sauli, ndi Sauli anabala Yonatani, ndi Malikisuwa, ndi Abinadabu, ndi Esbaala.
40 Ndipo mwana wa Yonatani ndiye Meribaala; ndi Meribaala anabala Mika.
41 Ndi ana a Mika: Pitoni, ndi Meleki, ndi Tareya, ndi Ahazi.
42 Ndi Ahazi anabala Yara, ndi Yara anabala Ameleti, ndi Azmaveti, ndi Zimri; ndi Zimri anabala Moza,
43 ndi Moza anabala Bineya, ndi Refaya mwana wace, Eleasa mwana wace; Azeli mwana wace;
44 ndi Azeli anali nao ana asanu ndi mmodzi, maina ao ndi awa; Azrikamu, Bokeru, ndi Ismayeli, ndi Seariya, ndi Obadiya, ndi Hanani; awa ndi ana a Azeli.