6 Ndi a ana a Zera: Yeueli ndi abale ao mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi anai.
7 Ndi a ana a Benjamini: Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Hodavia, mwana wa Hasenuwa;
8 ndi Ibineya mwana wa Yerohamu, ndi Ela mwana wa Uzi, mwana-wa Mikiri, ndi Mesulamu mwana wa Sefatiya, mwana wa Reueli, mwana wa Ibniya,
9 ndi abale ao monga mwa mibadwo yao mazana asanu ndi anai mphambu makumi asanu kudza asanu ndi mmodzi. Onsewa ndiwo akuru a nyumba za makolo ao m'nyumba za makolo ao.
10 Ndi a ansembe: Yedaya, ndi Yehoyaribu, ndi Yakini,
11 ndi Azariya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Merayoti, mwana wa Ahitubu, mtsogoleri wa m'nyumba ya Mulungu;
12 ndi Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pasuri, mwana wa Malikiya, ndi Maasai mwana wa Adieli, mwana wa Yazera, mwana wa Mesulamu, mwana wa Mesilemiti, mwana wa Imeri,