4 Iwowa adzakulankhulani, ndi kukupatsani mikate iwiri; imeneyi mudzailandira m'manja mwao.
5 Ndipo m'tsogolo mwace mudzafika ku phiri la Mulungu, kumene kuli kaboma ka Afilisti; ndipo kudzali kuti pakufika inu kumudziko mudzakomana ndi gulu la aneneri, alikutsika kumsanje ndi cisakasa, ndi lingaka, ndi toliro, ndi zeze, pamaso pao; iwo adzanenera;
6 ndipo Mzimu wa Yehova udzagwera inu kolimba, nanunso mudzanenera pamodzi nao, nimudzasandulika munthu wina.
7 Ndipo zitakufikirani zizindikilo izi mudzacita monga mudzaona pocita, pakuti Mulungu ali nanu.
8 Ndipo mudzatsika patsogolo pa ine kunka ku Giligala; ndipo, taonani, ndidzatsikira kwa inu kukapereka zopsereza, ndi kuphera nsembe zamtendere. Mutsotsepo masiku asanu ndi awiri kufikira ndikatsikira kwa inu ndi kukudziwitsani cimene mudzacita.
9 Ndipo kunali, pamene iye anapotoloka kuti alekane ndi Samueli, Mulungu anampatsa mtima wina watsopano; ndipo zizindikilo zija zonse zinacitika tsiku lija.
10 Ndipo pamene anafika kucitunda kuja, onani, gulu la aneneri linakomana naye; ndi Mzimu wa Mulungu unamgwera mwamphamvu, iye nanenera pakati pao,