6 Ndipo mzimu wa Mulungu unamgwera Sauli mwamphamvu, pamene anamva mau awa, ndi mkwiyo wace unayaka kwambiri.
7 Natenga ng'ombe ziwiri nazidula nthuli nthuli, nazitumiza m'malire monse mwa Israyeli, ndi dzanja la mithenga, nati, Amene sakudza pambuyo pa Sauli ndi pa Samueli, adzatero nazo ng'ombe zace. Ndipo kuopsa kwa Yehova kunawagwera anthu, naturuka ngati munthu mmodzi.
8 Ndipo anawawerenga ku Bezeki; ndipo ana a Israyeli anali zikwi mazana atatu, ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi makumi atatu.
9 Ndipo anati kwa mithenga inadzayi, Muzitero kwa anthu a ku Yabezi Gileadi, Mawa litatentha dzuwa, mudzaona cipulumutso. Ndipo mithenga inadza niuza a ku Yabezi; nakondwara iwowa.
10 Cifukwa cace anthu a ku Yabezi anati, Mawa tidzaturukira kwa inu, ndipo mudzaticitira cokomera inu.
11 Ndipo m'mawa mwace Sauli anagawa anthu magulu atatu; ndipo iwowa anafika pakati pa zithandozo m'ulonda wa mamawa, nakantha Aamoni kufikira kutentha kwa dzuwa. Ndipo otsalawo anabalalika, osatsala pamodzi ngakhale awiri.
12 Ndipo anthu anati kwa Samueli, Ndani iye amene anati, Kodi Sauli adzatiweruza ife? tengani anthuwo kuti tiwaphe.