1 Sauli anali ndi zaka makumi atatu pamene anayamba ufumu wace; nakhala mfumu ya Israyeli zaka ziwiri.
2 Pamenepo Sauli anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israyeli; zikwi ziwiri za iwowa zinali ndi Sauli ku Mikimasi, ndi ku phiri la ku Beteli; ndi cikwi cimodzi anali ndi Jonatani ku Gibeya wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao.
3 Ndipo Jonatani anathyola kaboma ka Afilisti lokhala ku Geba, ndipo Afilisti anamva za ici. Ndipo Sauli analiza lipenga m'dziko monse, nati, Amve Ahebri.
4 Ndipo Aisrayeli onse anamva kunena kuti Sauli anathyola kaboma ka Afilisti, ndi kuti Afilisti anyansidwa ndi Aisrayeli. Ndipo anthuwo anasonkhana kwa Sauli ku Giligala.