1 Ndipo kunali tsiku lina kuti Jonatani mwana wa Sauli ananena ndi mnyamata wonyamula zida zace, Tiye tipite kunka ku kaboma ka Afilisti, tsidya lija. Koma sanauza atate wace.
2 Ndipo Sauli analikukhala m'matsekerezo a Gibeya patsinde pa mtengo wankhangaza uli ku Migroni; ndipo panali naye anthu monga mazana asanu ndi limodzi;
3 ndi Ahiya mwana wa Ahitubi mbale wace wa Ikabodi, mwana wa Pinehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo, wobvala efodi. Ndipo anthuwo sanadziwa kuti Jonatani wacoka.
4 Ndipo pakati pa mipata imene Jonatani anafuna kupitapo kunka ku kaboma ka Afilisti, panali phiri lathanthwe pa mbali yina, ndi phiri lathanthwe pa mbali inzace; ndipo dzina la linalo ndilo Bozezi, ndi la linzace ndilo Sene.