3 ndi Ahiya mwana wa Ahitubi mbale wace wa Ikabodi, mwana wa Pinehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo, wobvala efodi. Ndipo anthuwo sanadziwa kuti Jonatani wacoka.
4 Ndipo pakati pa mipata imene Jonatani anafuna kupitapo kunka ku kaboma ka Afilisti, panali phiri lathanthwe pa mbali yina, ndi phiri lathanthwe pa mbali inzace; ndipo dzina la linalo ndilo Bozezi, ndi la linzace ndilo Sene.
5 Phiri lija linaimirira kuyang'ana kumpoto pandunji pa Mikimasi, ndi linzace kumwera pandunji pa Geba.
6 Ndipo Jonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zace, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira nchito; pakuti palibe comletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka.
7 Ndipo wonyamula zida zace ananena naye, Citani zonse ziri mumtima mwanu; palukani, onani ndiri pamodzi ndi inu monga mwa mtima wanu.
8 Ndipo Jonatani anati, Taona, ife tidzapita kunka kwa anthuwo, ndipo tidzadziu lula kwa iwo.
9 Akatero ndi ife kuti, Baimani kufikira titsikira kwa inu; tsono tidzaima m'malo mwathu, osakwera kwa iwo.