5 Ndipo Sauli anafika ku mudzi wa Amaleki, nalalira kucigwa.
6 Ndipo Sauli anauza Akeni kuti, Mukani, cokani mutsike kuturuka pakati pa Aamaleki, kuti ndingakuonongeni pamodzi ndi iwo; pakuti inu munacitira ana a Israyeli onse zabwino, pakufuma iwo ku Aigupto. Comwece Akeni anacoka pakati pa Aamaleki.
7 Ndipo Sauli anakantha Aamaleki, kuyambira pa Havila, dera la ku Suri; ciri pandunji pa Aigupto.
8 Namtenga wamoyo Agagi, mfumu ya Aamaleki, naononga konse konse anthu onse ndi lupanga lakuthwa.
9 Koma Sauli ndi anthu anamsunga wamoyo Agagi, ndi nkhosa zokometsetsa, ndi ng'ombe, ndi zonenepa zina, ndi ana a nkhosa, ndi zabwino zonse, sadafuna kuzitha psiti; koma zonse zoipa ndi zonyansa anaziononga konse konse.
10 Pamenepo mau a Yehova anafika kwa Samueli, nati,
11 Kundicititsa cisoni kuti ndinaika Sauli akhale mfumu; pakuti wabwerera wosanditsata Ine, ndipo sanacita malamulo anga, Ndipo Samueli anakwiya; nalira kwa Yehova usiku wonse.