9 Pamenepo Jese anapititsapo Sama. Ndipo anati, Koma uyunso Yehova sanamsankha.
10 Ndipo Jese anapititsapo ana ace amuna asanu ndi awiri. Koma Samueli anati kwa Jese, Yehova sanawasankha awa.
11 Ndipo Samueli anati kwa Jese, Ana anu ndi omwewa kodi? Nati iye, Watsala wina, mng'ono wa onse, ndipo taonani, iye alikuweta nkhosa. Ndipo Samueli anati kwa Jese, Tumiza munthu akamtenge; pakuti ife sitidzakhala pansi kufikira iye atadza kuno.
12 Ndipo anatumiza munthu, nabwera naye. Tsono iye anali wofiirira, ndi wa nkhope yokongola, ndi maonekedwe okoma. Ndipo Yehova anati, Nyamuka umdzoze, pakuti ndi ameneyu.
13 Pamenepo Samueli anatenga nyanga ya mafuta, namdzoza pakati pa abale ace; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli. Ndipo Samueli ananyamuka, Danks ku Rama.
14 Koma mzimu wa Yehova unamcokera Sauli, ndi mzimu woipa wocokera kwa Yehova unambvuta iye.
15 Ndipo anyamata a Sauli ananena naye, Onani tsopano, mzimu woipa wocokera kwa Mulungu ulikubvuta inu.