16 Ndipo Mfilistiyo anayandikira m'mawa ndi madzulo, nadzionetsera masiku makumi anai.
17 Ndipo Jese anati kwa Davide mwana wace, Uwatengere abale ako efa watirigu uyu wokazinga, ndi mikate iyi khumi, nuthamangire nazo kuzithando kwa abale ako;
18 nunyamule ncinci izi khumi zamase ukapatse mtsogoleri wa cikwi cao, nukaone m'mene akhalira abale ako, nulandire cikole cao,
19 Tsono Sauli, ndi iwowa, ndi anthu onse a Israyeli, anali m'cigwa ca Ela, ku nkhondo ya Afilisti.
20 Ndipo Davide anauka m'mamawa, nasiyira nkhosa wozisungira, nasenza zija, namuka, monga anamuuza Jese; ndipo iye anafika ku linga la magareta, napeza khamu lirikuturuka kunka poponyanira nkhondo lirikupfuula.
21 Ndipo Israyeli ndi Afilisti anandandalitsa nkhondo zao, khamu tina kuyang'anana ndi khamu lina.
22 Ndipo Davide anasiya akatundu ace m'dzanja la wosungira akatundu, nathamangira ku khamulo, nadza nalankhula abale ace.