23 Ndipo m'mene iye anali cilankhulire nao, onani cinakwerako ciwindaco, Mfilisti wa ku Gati, dzina lace ndiye Goliate, woturuka pakati pa mipambo ya Afilisti, nalankhula monga mau omwe aja; ndipo Davide anawamva.
24 Ndipo Aisrayeli onse, pakumuona munthuyo, anamthawa, naopa kwambiri.
25 Nati Aisrayeli, Kodi mwaona munthu uyu amene anakwera kuno? zoonadi iye anakwera kuti adzanyoze Israyeli, ndipo munthu wakumupha iye, mfumu idzamlemeza ndi cuma cambiri, nidzampatsa mwana wace wamkazi, nidzayesa nyumba ya atate wace yaufulu m'Israyeli.
26 Ndipo Davide analankhula ndi anthu akuima pafupi ndi iye, nati, Adzamcitira ciani munthu wakupha Mfilisti uyu, ndi kucotsa tonzo lace pakati pa Israyeli? pakuti Mfilisti uyu wosadulidwa ndiye yani, kuti azinyoza makamu a Mulungu wamoyo?
27 Ndipo anthuwo anamyankha motero, nati, Adzamcitira munthu wakumupha iye mwakuti mwakuti.
28 Ndipo Eliabu mkuru wace anamumva iye alikulankhula ndi anthu; ndipo Eliabu anapsa mtima ndi Davide, nati, Unatsikiranji kuno? ndi nkhosa zija zowerengeka unazisiya ndi yani, m'cipululu muja? Ine ndidziwa kudzikuza kwako ndi kuipa kwa mtima wako; pakuti watsika kuti udzaone nkhondoyi.
29 Ndipo Davide anati, Ndacitanji tsopano? Palibe cifukwa kodi?