27 Ndipo kunali tsiku laciwiri mwezi utakhala, Davide adasowekanso pamalo pace; ndipo Sauli anati kwa Jonatani mwana wace, Mwana wa Jese walekeranji kubwera kudya dzulo ndi lero lomwe?
28 Ndipo Jonatani anayankha Sauli, Davide anandiumiriza ndimlole amuke ku Betelehemu;
29 nati, Ndiloleni, ndimuke; cifukwa banja lathu lipereka nsembe m'mudzimo; ndi mbale wanga anandiuzitsa ndifikeko; tsono ngati wandikomera mtima undilole ndicoke, ndikaone abale anga. Cifukwa ca ici safika ku gome la mfumu.
30 Pamenepo Sauli anapsa mtima ndi Jonatani, nanena naye, Iwe mwana wa mkazi wa matsutso ndi wopikisana, sindidziwa kodi kuti wasankha mwana wa Jeseyo kudzinyaza wekha, ndi usiwa wa mai wako yemwe?
31 Popeza nthawi yonse mwana wa Jeseyo akhala ndi moyo padziko, koma sudzakhazikika iwe, kapena ufumu wako. Cifukwa cace tumiza tsopano numtengere kuno kwa ine, popeza adzafa ndithu,
32 Ndipo Jonatani anayankha Sauli atate wace, nanena, Aphedwe cifukwa ninji? anacitanji?
33 Ndipo Sauli anamponyera mkondo kuti amgwaze; momwemo Jonatani anazindikira kuti atate wace anatsimikiza mtima kupha Davide.