1 Ndipo Azifi anafika kwa Sauli ku Gibeya, nati, Kodi Davide sali kubisala m'phiri la Hagila, kupenya kucipululu!
2 Ndipo Sauli ananyamuka, natsikira ku cipululu ca Zifi, ndi anthu zikwi zitatu a Israyeli osankhika, kukafuna Davide m'cipululu ca Zifi.
3 Sauli namanga zithando m'phiri la Hagila kupenya kucipululu kunjira, Koma Davide anakhala kucipululu, naona kuti Sauli alikumfuna kucipululu komweko.
4 Cifukwa cace Davide anatumiza ozonda, nazindikira kuti Sauli anabwera ndithu,
5 Ndipo Davide ananyamuka nafika pamalo pala Sauli anamangapo; ndipo Davide adaona pogona Sauli, ndi Abineri mwana wa Neri kazembe wa khamu lace; ndipo Sauli anagona pakati pa linga la magareta, ndipo anthu adamanga zithando pomzinga pace.