1 Ndipo mwanayo Samueli anatumikira Yehova pamaso pa Eli. Ndipo masiku aja mau a Yehova anamveka kamodzi kamodzi; masomphenya sanaoneka-oneka.
2 Ndipo kunali nthawi yomweyo Eli atagona m'malo mwace (maso ace anayamba cizirezire osatha kupenya bwino);
3 ndi nyali ya Mulungu isanazime, Samueli nagona m'Kacisi wa Yehova, m'mene munali likasa la Mulungu.
4 Pamenepo Yehova anaitana Samueli; ndipo iye anayankha kuti, Ndiri pano.