7 Ndipo pamene anthu a ku Asidodi anaona kuti ncomweco, anati iwowa, Likasa la Mulungu wa Israyeli lisakhalitse ndi ife; popeza dzanja lace litiwawira ife, ndi Dagoni mulungu wathu.
8 Cifukwa cace anatumiza mithenga, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, nati, Ticite nalo ciani likasa la Mulungu wa Israyeli? Ndipo anati, Anyamule likasa la Mulungu kunka nalo ku Gati, Ndipo ananyamula likasalo la Mulungu wa Israyeli, napita nalo kumeneko.
9 Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mudziwo ndi kusautsa kwakukuru; ndipo anazunza anthu a mudziwo, akuru ndi ang'ono; ndi mafundo anawabuka.
10 Cifukwa cace anatumiza likasa la Mulungu ku Ekroni. Ndipo kunali pofika likasalo ku Ekroni, a ku Ekroni anapfuula nati, Anadzatitulira likasa la Mulungu wa Israyeli, kutipha ife ndi ana athu.
11 Cifukwa cace anatumiza, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, ndipo iwowa anati, Cotsani likasa la Mulungu wa Israyeli, lipitenso kumalo kwace, kuti lingationonge ife, ndi anthu athu; pakuti kunali kusautsa koopsa m'mudzi monse; dzanja la Mulungu linabvutadi pamenepo.
12 Ndipo amene anapanda kufa anagwidwa ndi mafundowo; ndi kulira kwa mudziwo kunakwera kumwamba.