1 Ndipo anthu a ku Kiriati-yearimu anabwera, natenga likasa la Yehova, nafika nalo m'nyumba ya Abinadabu paphiri; napatula mwana wace wamwamuna Eleazeri kuti asunge likasa la Yehova.
2 Ndipo kunali, kuti likasalo linakhala nthawi yaikuru m'Kiriati-yearimu; popeza linakhalako zaka makumi awiri; ndipo banja lonse la Israyeli linalirira Yehova.
3 Ndipo Samueli analankhula ndi banja lonse la Israyeli nati, Ngati mukuti mubwerere kunka kwa Yehova ndi mitima yanu yonse, cotsani pakati pa inu milungu yacilendo, ndi Asitaroti, nimukonzere Yehova mitima yanu, ndi kumtumikira iye yekha; mukatero, iye adzakupulumutsani m'manja a Afilisti.
4 Pomwepo ana a Israyeli anacotsa. Abaala ndi Asitaroti, natumikira Yehova yekha.