17 Idzatenga limodzi la magawo khumi la zoweta zanu; ndipo inu mudzakhala akapoloace.
18 Ndipotsiku lija mudzapfuula cifukwa ca mfumu yanu munadzisankhira nokha; koma Yehova sadzayankha inu tsiku lijalo.
19 Koma anthu anakana kumvera mau a Samueli; nati, Iai, koma tifuna kukhala nayo mfumu yathu;
20 kuti ifenso tikafanane nao anthu a mitundu yonse; kuti mfumu yathuyo ikatiweruzire, ndi kuturuka kutitsogolera, ndi kuponya nafe nkhondo zathu.
21 Ndipo Samueli anamva mau onse a anthuwo, nawafotokozanso m'makutu a Yehova.
22 Ndipo Yehova anati kwa Samueli, Umvere mau ao, nuwalongere mfumu, Ndipo Samueli anati kwa amuna a Israyeli, Mupite, munthu yense ku mudziwace.