10 Dziwani tsono, kuti sikadzagwa pansi kanthu ka mau a Yehova, amene Yehova ananena za nyumba va Ahabu; pakuti Yehova wacita cimene adanena mwa mtumiki wace Eliya.
11 Nawakantha Yehu otsala onse a nyumba ya Ahabu m'Yezreeli, ndi omveka ace onse, ndi odziwana naye, ndi ansembe ace, mpaka sanatsala wa iye ndi mmodzi yense.
12 Pamenepo ananyamuka, nacoka, namuka ku Samariya, Ndipo pokhala ku nyumba yosengera ya abusa panjira,
13 Yehu anakomana nao abale a Ahaziya mfumu ya Yuda, nati, Ndinu ayani? Nati iwo, Ife ndife abale a Ahaziya, tirikutsika kulankhulira ana a mfumu, ndi ana a nyumba yaikuru.
14 Nati iye, Agwireni amoyo. Nawagwira amoyo, nawapha ku dzenje la nyumba yosengera, ndiwo amuna makumi anai mphambu awiri; sanasiya ndi mmodzi yense.
15 Atacoka pamenepo, anakomana naye Yehonadabu mwana wa Rekabu wakudzamcingamira; namlankhula, nanena naye, Mtima wako ngwoongoka kodi, monga mtima wanga ubvomerezana nao mtima wako? Nati Yehonadabu, Momwemo. Ukatero undipatse dzanja lako. Nampatsa dzanja lace, namkweretsa pali iye pagareta.
16 Nati iye, Tiye nane, ukaone cangu canga ca kwa Yehova. M'mwemo anamuyendetsa m'gareta wace.