2 Tsono akakufikani inu kalata uyu, popeza muli nao ana a mbuye wanu; muli naonso magareta ndi akavalo, ndi mudzi walinga, ndi zida,
3 musankhe wokoma ndi woyenerayo wa ana a mbuye wanu, ndi kumuika pa mpando wacifumu wa atate wace; ndipo muiponyere nkhondo nyumba ya mbuye wanu.
4 Koma anaopa kwambiri, nati, Taonani, mafumu awiri sanaima pamaso pace, nanga ife tidzaima bwanji?
5 Ndipo iye wakuyang'anira nyumba, ndi iye wakuyang'anira mudzi, ndi akulu akulu, ndi iwo akulera anawo, anatumiza kwa Yehu, ndi kuti, Ife ndife akapolo anu ndi zonse mutiuza tidzacita; sitidzalonga munthu yense mfumu; cokomera pamaso panu citani.
6 Nawalembera kalata kaciwiri, nati, Mukakhala a ine ndi kumvera mau anga, tengani mitu va amunawo ana a mbuyewanu, ndi kundidzera ku Yezreeli mawa dzuwa lino. Koma ana a mfumu ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, anakhala ndi anthu omveka m'mudzi, amene anawalera.
7 Ndipo kunali, powafika kalatayo, anatenga ana a mfumu, nawapha amuna makumi asanu ndi awiri, naika mitu yao m'mitanga, naitumiza kwa iye ku Yezreeli.
8 Nudza mthenga, numfotokozera, kuti, Abwera nayo mitu va ana a mfumu. Nati iye, Mulunjike miulu iwiri polowera pa cipata kufikira m'mawa.