2 Koma Yoseba mwana wa mfumu Yoramu, mlongo wace wa Ahaziya, anatenga Yoasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu akuti aphedwe, iye ndi mlezi, nawaika m'cipinda cogonamo; nambisira Ataliya, ndipo sanaphedwa.
3 Nakhala naye wobisika m'nyumba ya Yehova zaka zisanu ndi cimodzi; ndipo Ataliya anakhala mfumu ya dziko.
4 Koma caka cacisanu ndi ciwiri Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a mazana a opha anthu, ndi a otumikira, nabwera nao kwa iye ku nyumba ya Yehova, napangana nao, nawalumbiritsa m'nyumba ya Yehova, nawaonetsa mwana wa mfumu.
5 Nawalamulira, kuti, Cocita inu ndi ici: limodzi la magawo atatu la inu olowa pa Sabata lizilindira nyumba ya mfumu,
6 ndi lina lizikhala ku cipata ca Suri, ndi lina ku cipata kumbuyo kwa otumikira; momwemo muzisunga nyumba, ndi kuicinjiriza.
7 Ndipo magawo awiri ainu, ndiwo onse oturukira pa Sabata, azilindira nyumba ya Yehova kuzinga mfumu.
8 Ndipo muzizinga mfumu, yense zida zace m'manja mwace, ndi iye wakulowa poima inupo aphedwe; ndipo muzikhala inu ndi mfumu poturuka ndi polowa iye.