24 Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, sanaleka zolakwa zonse za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli.
25 Anabweza malire a Israyeli kuyambira polowera ku Hamati mpaka nyanja ya kucidikha, monga mwa mau a Yehova Mulungu wa Israyeli, amene ananena ndi dzanja la mtumiki wace Yona mwana wa Amitai mneneriyo, ndiye wa Gati-heferi,
26 Pakuti Yehova anapenya kuti kuzunzika kwao kwa Israyeli nkowawa ndithu; popeza panalibe womangika kapena womasuka, ndipo panalibe womthandiza Israyeli.
27 Ndipo Yehova sadanena kuti adzafafaniza dzina la Israyeli pansi pa thambo; koma anawapulumutsa ndi dzanja la Yerobiamu mwana wa Yoasi.
28 Macitidwe ena tsono a Yerobiamu, ndi zonse anazicita, ndi mphamvu yace, umo anacita nkhondo, nabweza kwa Israyeli Damasiko ndi Hamati amene anali a Yuda, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?
29 Ndipo Yerobiamu anagona ndi makolo ace, ndiwo mafumu a Israyeli; nakhala mfumu m'malo mwace Zekariya mwana wace.