1 Ndipo kunali caka cacitatu ca Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israyeli, Hezekiya mwana wa Ahazi mfumu ya Yuda analowa ufumu waceo
2 Ndiye wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Abi mwana wa Zekariya.
3 Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazicita Davide kholo lace.
4 Anacotsa misanje, naphwanya zoimiritsa, nalikha cifanizo, naphwanya njoka ija yamkuwa adaipanga Mose; pakuti kufikira masiku awa ana a Israyeli anaifukizira zonunkhira, naicha Cimkuwa.
5 Anakhulupirira Yehova Mulungu wa Israyeli; atafa iye panalibe wakunga iye mwa mafumu onse a Yuda, ngakhale mwa iwo okhalapo asanabadwe iye.
6 Pakuti anaumirira Yehova osapambuka pambuyo pace, koma anasunga malamulo amene Yehova adawalamulira Mose.
7 Ndipo Yehova anali naye, nacita iye mwanzeru kuli konse anamukako, napandukira mfumu ya Asuri osamtumikira.