13 Caka cakhumi ndi zinai ca Hezekiya Sanakeribu mfumu ya Asuri anakwerera midzi yonse ya malinga ya Yuda, nailanda.
14 Natumiza Hezekiya mfumu ya Yuda kwa mfumu ya Asuri ku Lakisi, ndi kuti, Ndalakwa; mundicokere; cimene mundisenzetse ndisenza. Pamenepo mfumu ya Asuri anaikira Hezekiya mfumu ya Yuda matalente mazana atatu a siliva ndi matalente makumi atatu a golidi.
15 Napereka Hezekiya siliva yense wopezeka m'nyumba ya Yehova, ndi ku cuma ca nyumba yamfumu.
16 Nthawi yomweyi Hezekiya anakanganula golidi wa pa zitseko za Kacisi wa Yehova, ndi pa zimphuthu adazikuta Hezekiya mfumu ya Yuda, nampereka kwa mfumu ya Asuri.
17 Ndipo mfumu ya Asuri anatuma nduna ndi ndoda ndi kazembe ocokera ku Lakisi ndi khamu lalikuru la nkhondo kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Nakwera iwo, nafika ku Yerusalemu. Ndipo atakwera, anafika, naima ku mcerenje wa thamanda la kumtunda, ndilo la ku mseu wa ku mwaniko wa otsuka nsaru.
18 Ndipo m'mene adaitana mfumu, anawaturukira Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba ya mfumu, ndi Sebina mlembi, ndi Yoa mwana wa Asafu wolemba mbiri.
19 Nanena nao kazembeyo, Muuzetu Hezekiya, Itero mfumu yaikuru, mfumu ya Asuri, Cikhulupiriro ici ncotani ucikhulupirira?