3 Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazicita Davide kholo lace.
4 Anacotsa misanje, naphwanya zoimiritsa, nalikha cifanizo, naphwanya njoka ija yamkuwa adaipanga Mose; pakuti kufikira masiku awa ana a Israyeli anaifukizira zonunkhira, naicha Cimkuwa.
5 Anakhulupirira Yehova Mulungu wa Israyeli; atafa iye panalibe wakunga iye mwa mafumu onse a Yuda, ngakhale mwa iwo okhalapo asanabadwe iye.
6 Pakuti anaumirira Yehova osapambuka pambuyo pace, koma anasunga malamulo amene Yehova adawalamulira Mose.
7 Ndipo Yehova anali naye, nacita iye mwanzeru kuli konse anamukako, napandukira mfumu ya Asuri osamtumikira.
8 Anakantha Afilisti mpaka Gaza ndi malire ace, kuyambira nsanja ya olonda mpaka mudzi walinga.
9 Ndipo kunali caka cacinai ca mfumu Hezekiya, ndico caka cacisanu ndi ciwiri ca Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israyeli Salimanezeri mfumu ya Asuri anakwerera Samariya, naumangira misasa.