31 Musamvere Hezekiya; pakuti Itero mfumu ya Asuri, Mupangane nane zamtendere, nimuturukire kwa ine, ndi kumadya yense ku mpesa wace, ndi yense ku mkuyu wace, ndi kumwa yense madzi a m'citsime cace;
32 mpaka ndifika ndi kumuka nanu ku dziko lakunga dziko lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la mkate ndi minda yampesa, dziko la azitona ndi la uci; kuti mukhale ndi moyo osafai; nimusamvere Hezekiya akakukopani, ndi kuti, Yehova adzatilanditsa.
33 Kodi mlungu uli wonse wa amitundu walanditsa dziko lace m'dzanja la mfumu ya Asuri ndi kale lonse?
34 Iri kuti milungu ya Hamati, ndi ya Aripadi? iri kuti milungu ya Sefaravaimu, kapena Hena, ndi Iva? Kodi yalanditsa Samariya m'dzanja langa?
35 Ndi yiti mwa milungu yonse ya maiko inalanditsa maiko ao m'dzanja langa, kuti Yehova adzalanditsa Yerusalemu m'dzanja langa?
36 Koma anthuwo anakhala cete osamyankha mau; pakuti lamulo la mfumu ndilo kuti, Musamuyankha.
37 Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba, ndi Sebina mlembi, ndi Yoa mwana wa Asafu wolembera mbiri, anadza kwa Hezekiya ndi zobvala zao zong'ambika, namuuza mau a kazembeyo.