16 Cherani khutu lanu, Yehova, nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimupenye; ndipo imvani mau a Sanakeribu, amene anatumiza kutonza nao Mulungu wamoyo.
17 Zoona, Yehova, mafumu a Asuri anapasula amitundu ndi maiko ao,
18 naponya milungu yao kumoto; popeza sindiyo milungu koma yopanga anthu ndi manja ao, mtengo ndi mwala; cifukwa cace anaiononga.
19 Ndipo tsono, Yehova Mulungu wathu, mutipulumutse m'dzanja lace, kuti adziwe maufumu onse a dziko lapansi kuti Inu ndinu Yehova Mulungu, Inu nokha nokha.
20 Pamenepo Yesaya mwana wa Amozi anatumiza kwa Hezekiya, ndi, kuti, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Condipempha iwe pa Sanakeribu mfumu ya Asuri ndacimva.
21 Mau a Yehova akumnenera iye ndi awa, Namwali mwana wamkazi wa Ziyoni akunyoza, akuseka mwana wamkazi wa Yerusalemu, akupukusira mutu pambuyo pako.
22 Ndiye yani wamtonza ndi kumcitira mwano? ndiye yani wamkwezera mau ndi kumgadamira maso ako m'mwamba? Ndiye Woyerayo wa Israyeli.