7 Koma mfumu ya Aigupto sinabwerezanso kuturuka m'dziko lace, pakuti mfumu ya Babulo idalanda kuyambira ku mtsinje wa Aigupto kufikira ku mtsinje Firate, ndilo lonse anali nalo mfumu ya Aigupto.
8 Yoyakini anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu polowa iye ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu miyezi itatu; ndi dzina la mace ndiye Nehusita mwana wa Elinatani wa ku Yerusalemu.
9 Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, monga umo monse adacita atate wace.
10 Nthawi ija anyamata a Nebukadinezara mfumu ya Babulo anakwerera Yerusalemu, naumangira mudziwo misasa.
11 Nafika Nebukadinezara mfumu ya Babulo kumudzi, ataumangira misasa anyamata ace,
12 ndipo Yoyakini mfumu ya Yuda anaturukira kwa mfumu ya Babulo, iye ndi mace, ndi anyamata ace, ndi akalonga ace, ndi adindo ace; mfumu ya Babulo nimtenga caka cacisanu ndi citatu ca ufumu wace.
13 Naturutsa kucotsa komweko cuma conse ca nyumba ya Yehova, ndi cuma ca nyumba ya mfumu, naduladula zipangizo zonse zagolidi adazipanga Solomo mfumu ya Israyeli m'Kacisi wa Yehova, monga Yehova adanena.