1 Ndipo Namani kazembe wa khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu anali munthu womveka pamaso pa mbuyace, ndi waulemu; popeza mwa iye Yehova adapulumutsa Aaramu; ndiyenso ngwazi, koma wakhate.
2 Ndipo Aaramu adaturuka magulu magulu, nabwera nalo m'ndende buthu locokera ku dziko la Israyeli, natumikira mkazi wa Namani iyeyu,
3 Nati uyu kwa mbuyace wamkazi, Mbuye wanga akadakhala kwa mneneri ali m'Samariya, akadamciritsa khate lace.
4 Ndipo analowa wina, nauza mbuye wace, kuti, Buthulo lofuma ku dziko la Israyeli lanena zakuti zakuti.
5 Pamenepo mfumu ya Aramu inati, Tiye, muka, ndidzatumiza kalata kwa mfumu ya Israyeli. Pamenepo anacoka, atatenga siliva: matalente khumi, ndi golidi masekeli zikwi zisanu ndi cimodzi, ndi zobvala zakusintha khumi.