1 Ndipo Elisa mneneriyo anaitana mmodzi wa ana a aneneri, nanena naye, Udzimangire m'cuuno, nutenge nsupa iyi ya mafuta m'dzanja mwako, numuke ku Ramoti Gileadi.
2 Ndipo ukafikako, ukaunguzeko Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimsi, nulowe numnyamukitse pakati pa abale ace, nupite naye ku cipinda cam'katimo.
3 Nutenge nsupa ya mafutayo, nuwatsanulire pamutu pace, nunene, Atero Yehova; Ndakudzoza iwe ukhale mfumu pa Israyeli. Utatero, tsegula pakhomo, nuthawe osacedwa,
4 Pamenepo mnyamatayo, ndiye mneneri, anamuka ku Ramoti Gileadi.
5 Nalowa, ndipo taonani, akazembe a khamu alikukhala pansi; nati iye, Ndiri ndi mau kwa inu, kazembe. Nati Yehu, Kwa yani wa ife tonse? Nati iye, Kwa Inu, kazembe.
6 Nanyamuka, nalowa m'nyumba; ndipo anatsanulira mafutawo pamutu pace, nanena naye, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Ndakudzoza ukhale mfumu ya pa anthu a Yehova, ndiwo Aisrayeli.