4 Pamenepo mnyamatayo, ndiye mneneri, anamuka ku Ramoti Gileadi.
5 Nalowa, ndipo taonani, akazembe a khamu alikukhala pansi; nati iye, Ndiri ndi mau kwa inu, kazembe. Nati Yehu, Kwa yani wa ife tonse? Nati iye, Kwa Inu, kazembe.
6 Nanyamuka, nalowa m'nyumba; ndipo anatsanulira mafutawo pamutu pace, nanena naye, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Ndakudzoza ukhale mfumu ya pa anthu a Yehova, ndiwo Aisrayeli.
7 Nudzakantha nyumba ya Ahabu mbuye wako, kuti ndibwezere cilango ca mwazi wa: atumiki anga aneneri, ndi mwazi wa atumiki onse a Yehova, dzanja la Yezebeli.
8 Popeza nyumba yonse ya Ahabu idzaonongeka, ndipo ndidzalikhira Ahabu ana amuna onse womangika ndi womasuka m'Israyeli.
9 Ndipo ndidzalinganiza nyumba ya Ahabu ndi nyumba ya Yerobiamu mwana wa Nebati, ndi nyumba ya Basa mwana wa Ahiya.
10 Ndipo agaru adzamudya Yezebeli pa dera la Yezreeli, wopanda wina wakumuika. Pamenepo anatsegula pakhomo, nathawa.